Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Timoteyo 3:11 - Buku Lopatulika

11 mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira m'Antiokeya, m'Ikonio, m'Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 mazunzo anga, masautso anga, monga zinandichitikira ku Antiokeya, ku Ikoniya ndi ku Lusitra. Ndinazunzika kwambiri. Koma Ambuye anandipulumutsa pa zonsezi.

Onani mutuwo Koperani




2 Timoteyo 3:11
43 Mawu Ofanana  

mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.


Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo.


Amene anditulutsa kwa adani anga; inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa.


Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.


Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa; awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa, chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.


Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.


Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.


Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.


Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m'mwamba ndi padziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango.


Koma iwowa, atapita pochokera ku Perga anafika ku Antiokeya wa mu Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi.


Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.


Ndipo pa Listara panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwake, wopunduka chibadwire, amene sanayende nthawi zonse.


wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;


Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga.


ndi kukulanditsa kwa anthu, ndi kwa amitundu, amene Ine ndikutuma kwa iwo,


Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang'ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika;


pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambiri ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa.


kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;


Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu.


Ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo.


Chifukwa chake ndisangalala m'mafooko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, chifukwa cha Khristu; pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.


Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro:


Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa