Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Timoteyo 1:18 - Buku Lopatulika

18 (Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri mu Efeso, uzindikira iwe bwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 (Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri m'Efeso, uzindikira iwe bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ambuye amulole kuti adzalandire chifundo kwa Mulungu pa tsiku la chiweruzo. Ukudziŵa bwino ndi iwe wemwe kuti adandithandiza kwambiri ku Efeso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ambuye amulole kuti adzalandire chifundo kwa Ambuye pa tsiku lijalo! Ukudziwa bwino momwe iye anandithandizira mʼnjira zosiyanasiyana ku Efeso.

Onani mutuwo Koperani




2 Timoteyo 1:18
26 Mawu Ofanana  

Nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, kodi mwamgwetsera choipa mkazi wamasiye amene ndikhala naye, kumphera mwanake?


Kuchitira atate athu chifundo, ndi kukumbukira pangano lake lopatulika;


chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu wathu. M'menemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife.


ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao.


Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.


koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.


Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena;


amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira chimaliziro, kuti mukhale opanda chifukwa m'tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.


Koma ndidzakhala ku Efeso kufikira Pentekoste.


ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.


Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu;


koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,


Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwake?


Monga ndinakudandaulira iwe utsalire mu Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,


Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.


Ambuye achitire banja la Onesifore chifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawirikawiri, ndipo sanachite manyazi ndi unyolo wanga;


komatu pokhala mu Roma iye anandifunafuna ine ndi khama, nandipeza.


Koma Tikiko ndamtuma ku Efeso.


chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake.


pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.


Kunena za chipulumutso ichi anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za chisomo chikudzerani;


Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba: Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa