Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Petro 3:7 - Buku Lopatulika

7 koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chionongeko cha anthu osapembedza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chionongeko cha anthu osapembedza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Koma Mulungu ndi mau omwe aja adasunga zakuthambo ndi dziko lapansi la masiku ano kuti adzazitenthe ndi moto. Akuzisunga kufikira tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osasamala za Iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




2 Petro 3:7
31 Mawu Ofanana  

Zidzatha izi, koma Inu mukhala: Inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika:


Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete. Moto udzanyeka pankhope pake, ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.


Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi padziko pakuti kumwamba kudzachoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati chofunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa ngati njenjete; koma chipulumutso changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chilungamo changa sichidzachotsedwa.


Pakuti taonani, Yehova adzafika m'moto, ndi magaleta ake adzafanana ndi kamvulumvulu; kubwezera mkwiyo wake ndi ukali, ndi kudzudzula ndi malawi amoto.


Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbuu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pamutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka.


Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.


Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.


Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umenewo.


Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza mlandu wao wa Tiro ndi Sidoni udzachepa ndi wanu.


Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa ndi wako.


Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza.


Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.


Iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye, mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza.


Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;


ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.


osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;


munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chafika chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,


Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m'chiyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'chionongeko ndi chitayiko.


Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.


Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;


Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.


akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m'menemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam'mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.


M'menemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tili ife m'dziko lino lapansi.


Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.


Ndipo chilombo chinalicho, ndi kulibe, icho chomwe ndicho chachisanu ndi chitatu, ndipo chili mwa zisanu ndi ziwirizo, ndipo chinamuka kuchitayiko.


Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa