Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Petro 3:1 - Buku Lopatulika

1 Okondedwa, iyi ndiye kalata yachiwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Okondedwa, uyu ndiye kalata wachiwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Inu okondedwa, kalata ndikukulemberaniyi ndi yachiŵiri. M'makalata aŵiri onseŵa ndafuna kuutsa mitima yanu kuti mukhale ndi maganizo oona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Inu okondedwa, iyi ndi kalata yanga yachiwiri kwa inu. Ine ndalemba makalata onse awiri kuti ndikukumbutseni ndi kukutsitsimutsani ndi cholinga choti muzilingalira moyenera.

Onani mutuwo Koperani




2 Petro 3:1
15 Mawu Ofanana  

Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga.


Indedi Mulungu achitira Israele zabwino, iwo a mtima wa mbee.


Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu.


Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kachiwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adachimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka;


Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.


Chifukwa chake ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe mwa kuika kwa manja anga.


Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu zili zoposa ndi zophatikana chipulumutso, tingakhale titero pakulankhula;


Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;


Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;


Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.


Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.


Koma ichi chimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.


Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa