Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Petro 2:8 - Buku Lopatulika

8 (pakuti wolungamayo pokhala pakati pao. Ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zao zosaweruzika).

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 (pakuti wolungamayo pokhala pakati pao. Ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zao zosaweruzika).

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Munthu wolungama uja, pokhala pakati pao, analikumva ndi kuwona machitidwe ao oipa, ndipo tsiku ndi tsiku mtima wake wolungama unkavutikadi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 (Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva).

Onani mutuwo Koperani




2 Petro 2:8
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.


Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.


Changu changa chinandithera, popeza akundisautsa anaiwala mau anu.


Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao; popeza sasamalira mau anu.


Monga kasupe wopondedwa, ndi chitsime choonongeka, momwemo wolungama ngati agonjera woipa.


Posekera olungama pali ulemerero wambiri; koma pouka oipa anthu amabisala.


Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mzinda, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.


iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro, ndipo muyambe pamalo anga opatulika. Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.


podziwa ichi, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osaweruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,


Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa