Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Petro 1:12 - Buku Lopatulika

12 Mwa ichi sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m'choonadi chili ndi inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Mwa ichi sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m'choonadi chili ndi inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Nchifukwa chake cholinga changa nchakuti ndizikukumbutsani zimenezi nthaŵi zonse, ngakhale mukuzidziŵa ndipo mumakhulupirira ndi mtima wonse choona chimene mudalandira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Tsono ine ndidzakukumbutsani nthawi zonse za zinthu zimenezi, ngakhale kuti mumazidziwa ndipo kuti munakhazikika mʼchoonadi chimene muli nacho tsopano.

Onani mutuwo Koperani




2 Petro 1:12
20 Mawu Ofanana  

Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'chikhulupiriro, nachuluka m'chiwerengo chao tsiku ndi tsiku.


Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundivuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa.


chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu mu Mwamba, chimene mudachimva kale m'mau a choonadi cha Uthenga Wabwino,


ozika mizu ndi omangiririka mwa Iye, ndi okhazikika m'chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko.


Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa m'mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;


Chifukwa chake ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe mwa kuika kwa manja anga.


Koma tadzikumbutsani masiku akale, m'menemo mutaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zowawa;


Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.


Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.


Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo.


Ndipo ndichiyesa chokoma, pokhala ine m'msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;


Koma ndidzachitanso changu kosalekeza kuti nditachoka ine, mudzakhoza kukumbukira izi.


Okondedwa, iyi ndiye kalata yachiwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani;


Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.


Sindinakulembereni chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi.


chifukwa cha choonadi chimene chikhala mwa ife, ndipo chidzakhala ndi ife ku nthawi yosatha:


Koma inu, abale, mukumbukire mau onenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu;


Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.


Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa