Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 9:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wake; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Sheba anapatsa mfumu Solomoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wake; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Sheba anapatsa mfumu Solomoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Itanena zimenezo mfumukaziyo idapatsa mfumu Solomoni golide wa makilogramu 4,000, zonunkhira zambirimbiri ndiponso miyala yamtengowapatali. Nkale lonse sikudaoneke zokometsera chakudya zonga zimene mfumukazi ya ku Sheba idapatsa mfumu Solomoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kenaka iyo inapereka kwa mfumu makilogalamu 4,000 a golide, zonunkhira zambirimbiri ndi miyala yokongola. Nʼkale lomwe sikunaonekenso zonunkhiritsa ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapereka kwa mfumu Solomoni.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 9:9
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;


Ndipo mkaziyo ananinkha mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zaunyinji ndi timiyala ta mtengo wapatali; sunafikenso unyinji wotero wa zonunkhira wolingana ndi uja mfumu yaikazi ya ku Sheba inapereka kwa mfumu Solomoni.


Ndipo Hiramu adatumiza kwa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri.


Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni, anadza kumuyesera Solomoni ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukulu, ndi ngamira zosenza zonunkhira, ndi golide wochuluka, ndi timiyala ta mtengo wake; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.


Ndiponso anyamata a Huramu, ndi anyamata a Solomoni otenga golide ku Ofiri, anatenga mitengo yambawa ndi timiyala ta mtengo wapatali.


Nabwera nao munthu yense mtulo wake, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolide, zovala, ndi zida za nkhondo, ndi mure, akavalo ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka.


Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wake, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ake; popeza Mulungu wanu anakonda Aisraele kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kuchita chiweruzo ndi chilungamo.


Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.


Ndipo iye adzakhala ndi moyo; ndipo adzampatsa golide wa ku Sheba; nadzampempherera kosalekeza; adzamlemekeza tsiku lonse.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi lubani loona; miyeso yofanana;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa