2 Mbiri 9:6 - Buku Lopatulika6 Koma sindinakhulupirire mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zochuluka; mwaonjezatu pa mbiri ndidaimva. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Koma sindinakhulupirira mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zochuluka; mwaonjezatu pa mbiri ndidaimva. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Zimenezo sindidazikhulupirire, mpaka nditafika ndikuona chamaso. Ndipotu anthu sadaandiuzeko zonse ngakhale ndi theka lomwe la nzeru zanu zonse. Mukupambana kutali mbiri imene ndidaaimva. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Koma sindinakhulupirire zimene ankanena mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe la kuchuluka kwa nzeru zanu, pakuti zaposa zimene ndinamva. Onani mutuwo |