Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 9:4 - Buku Lopatulika

4 ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi mavalidwe ao, ndi makweredwe ake pokwera iye kunka kunyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi mavalidwe ao, ndi makweredwe ake pokwera iye kunka kunyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 chakudya cha patebulo pake, m'mene zinkakhalira nduna zake, m'mene ankasungira mwambo atumiki ake ndi zovala zao, atumiki ake operekera zakumwa ndi zovala zao, ndiponso nsembe zake zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Chauta, mfumukaziyo idangoti kukamwa pululu, kusoŵa chonena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo; atumiki opereka zakumwa ndi zovala zawo ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 9:4
22 Mawu Ofanana  

ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi zovala zao, ndi otenga zikho ake, ndi nsembe yake yopsereza imene amapereka m'nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo.


Ndipo Solomoni anatumiza mau kwa Hiramu, nati,


Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake.


Nachotsa kunyumba ya Yehova malo ophimbika a pa Sabata adawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, chifukwa cha mfumu ya Asiriya.


amene adadikira pa chipata cha mfumu kum'mawa mpaka pomwepo, ndiwo odikira pakhomo a tsasa la ana a Levi.


napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yake polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oimbira omwe analiko ndi zoimbirazo, nalangiza poimbira cholemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nati, Chiwembu, chiwembu.


Ndipo mfumu yaikazi ya ku Sheba ataiona nzeru ya Solomoni, ndi nyumba adaimanga,


Ndipo anati kwa mfumu, Inali yoona mbiri ija ndidaimva m'dziko langa, ya machitidwe anu, ndi ya nzeru zanu.


Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.


Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba chipulumutso chanu: Ndinayembekezera mau anu.


Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.


Tiyeni, idyani chakudya changa; nimumwe vinyo wanga ndamsakaniza.


Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani? Kuti ndadwala ndi chikondi.


Koma kunena za kalonga, iye akhale m'menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe kunjira ya kukhonde la chipata, natulukire njira yomweyi.


Ndipo kalonga azilowera njira ya kukhonde la chipatacho, kunja kwake, naime kunsanamira ya chipata; ndipo ansembe akonze nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, nalambire iye kuchiundo cha chipata; atatero atuluke; koma pachipata pasatsekedwe mpaka madzulo.


Pakuti mnyamata wa mbuye wanga inu akhoza bwanji kulankhula ndi mbuye wanga inu? Pakuti ine tsopano apa mulibenso mphamvu mwa ine, osanditsaliranso mpweya.


koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake wonse sanavale monga limodzi la amenewa.


Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.


Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,


Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa