Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 9:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Solomoni anammasulira mau ake onse, panalibe kanthu kombisikira Solomoni, kamene sanammasulire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Solomoni anammasulira mau ake onse, panalibe kanthu kombisikira Solomoni, kamene sanammasulire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Solomoni adayankha mafunso ake onse. Panalibe kanthu kalikonse kobisika kwa Solomoniyo, kamene sadathe kuimasulira mfumukaziyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta kwa iye komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 9:2
12 Mawu Ofanana  

taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.


Ndipo Mulungu anampatsa Solomoni nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziwa za mitundumitundu, zonga mchenga uli m'mphepete mwa nyanja.


Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni, anadza kumuyesera Solomoni ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukulu, ndi ngamira zosenza zonunkhira, ndi golide wochuluka, ndi timiyala ta mtengo wake; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.


Ndipo mfumu yaikazi ya ku Sheba ataiona nzeru ya Solomoni, ndi nyumba adaimanga,


Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.


Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya; kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.


Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zichitidwa m'mafanizo;


ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake.


Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.


amene zolemera zonse za nzeru ndi chidziwitso zibisika mwa Iye.


Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.


Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa