Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 9:16 - Buku Lopatulika

16 Napanganso malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera masekeli mazana atatu a golide; ndipo mfumu inazilonga m'nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Napanganso malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera masekeli mazana atatu a golide; ndipo mfumu inazilonga m'nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Adapanganso zishango 300 zazing'ono za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide wokwanira makilogramu atatu. Tsono mfumu idaika zishangozo m'Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Iye anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide wosasantha ndipo chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu. Mfumu inayika zishangozi mʼnyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 9:16
5 Mawu Ofanana  

nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; inde anachotsa chonsecho, nachotsanso zikopa zagolide zonse adazipanga Solomoni.


Anamanganso nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni, m'litali mwake munali mikono zana limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo.


Ndipo Sisake mfumu ya Aejipito anakwerera Yerusalemu, nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; anazichotsa zonse; anachotsanso zikopa zagolide adazipanga Solomoni.


Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri za golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera golide wonsansantha masekeli mazana awiri.


Mfumu inapanganso mpando wachifumu waukulu wa minyanga, naukuta ndi golide woona.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa