Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 9:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni, anadza kumuyesera Solomoni ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukulu, ndi ngamira zosenza zonunkhira, ndi golide wochuluka, ndi timiyala ta mtengo wake; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni, anadza kumuyesera Solomoni ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukulu, ndi ngamira zosenza zonunkhira, ndi golide wochuluka, ndi timiyala ta mtengo wake; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mfumukazi ya ku Sheba itamva za mbiri ya Solomoni, idadza ku Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso apatali. Idabwera ndi atumiki ambiri ndi ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yamtengowapatali. Itafika kwa Solomoni, idamuuza zonse za kumtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni, inabwera mu Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso okhwima. Inafika ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri, ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 9:1
23 Mawu Ofanana  

ndi Obala, ndi Abimaele, ndi Sheba;


Ndi ana aamuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedani.


Ndipo Yokisani anabala Sheba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi.


Pakuti anali wanzeru woposa anthu onse, woposa Etani wa ku Ezara, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Darida ana a Maholi; ndipo mbiri yake inafikira amitundu onse ozungulira.


Ndipo Solomoni mwana wa Davide analimbikitsidwa mu ufumu wake, ndipo Yehova Mulungu wake anali naye, namkuza kwakukulu.


nzeru ndi chidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhale nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.


Ndipo Solomoni anammasulira mau ake onse, panalibe kanthu kombisikira Solomoni, kamene sanammasulire.


Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wake; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Sheba anapatsa mfumu Solomoni.


Nditsanulira kudandaula kwanga pamaso pake; ndionetsa msauko wanga pamaso pake.


Ndidzatchera khutu kufanizo, ndidzafotokozera chophiphiritsa changa poimbira.


Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.


Ndipo iye adzakhala ndi moyo; ndipo adzampatsa golide wa ku Sheba; nadzampempherera kosalekeza; adzamlemekeza tsiku lonse.


Ndidzatsegula pakamwa panga mofanizira; ndidzatchula zinsinsi zoyambira kale.


kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lake, mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.


Gulu la ngamira lidzakukuta, ngamira zazing'ono za Midiyani ndi Efa; iwo onsewo adzachokera ku Sheba adzabwera nazo golide ndi lubani; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.


Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.


Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye anachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomoni; ndipo onani, wakuposa Solomoni ali pano.


Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.


kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri, kuti, Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo; ndidzawulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi.


Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.


Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza kuchokera kumalekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomoni; ndipo onani, woposa Solomoni ali pano.


Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndili mkazi wa mtima wachisoni; sindinamwe vinyo kapena chakumwa chowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa