2 Mbiri 8:6 - Buku Lopatulika6 ndi Baalati, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi mizinda yonse ya magaleta ake, ndi mizinda ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa mu Yerusalemu, ndi mu Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 ndi Baalati, ndi midzi yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi midzi yonse ya magaleta ake, ndi midzi ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa m'Yerusalemu, ndi m'Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Adamanganso Baalati ndiponso mizinda yonse yosungiramo zinthu zimene anali nazo, mizinda yonse yosungiramo magaleta ake, ndi ina yomakhalamo anthu ake okwera pa akavalo, ndi zonse zimene Solomoni adafuna kuti amange ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene Solomoni ankaŵalamulira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 pamodzinso ndi Baalati ndi mizinda yake yonse yosungira chuma, ndiponso mizinda yonse yosungiramo magaleta ake ndi akavalo ndi chilichonse anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira. Onani mutuwo |