Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 8:5 - Buku Lopatulika

5 Anamanganso Betehoroni wa kumtunda, ndi Betehoroni wa kunsi, mizinda ya malinga yokhala nao malinga, zitseko, ndi mipiringidzo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Anamanganso Betehoroni wa kumtunda, ndi Betehoroni wa kunsi, midzi ya malinga yokhala nao malinga, zitseko, ndi mipiringidzo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adamanganso Betehoroni wakumtunda ndi Betehoroni wakunsi, mizinda yamalinga yokhala ndi makoma, zitseko ndi mipiringidzo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Anamanganso Beti-Horoni Wakumtunda ndi Beti-Horoni Wakumunsi, mizinda yotetezedwa yokhala ndi makoma, zitseko ndi zitsulo zotchingira,

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 8:5
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anamanganso Gezere, ndi Betehoroni wakunsi,


Ndipo mwana wake wamkazi ndiye Seera, amene anamanga Betehoroni wa kunsi, ndi Betehoroni wa kumtunda, ndi Uzeniseera.


Ndipo anati kwa Yuda, Timange mizinda iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosavutika.


Ndipo anamanga Tadimori m'chipululu, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma, imene anaimanga mu Hamati.


ndi Baalati, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi mizinda yonse ya magaleta ake, ndi mizinda ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa mu Yerusalemu, ndi mu Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.


natsikira kumadzulo kunka ku malire a Ayafileti, ku malire a Betehoroni wa kunsi, ndi ku Gezere; ndi matulukiro ake anali kunyanja.


Ndipo malire a ana a Efuremu, monga mwa mabanja ao, ndiwo: malire a cholowa chao kum'mawa ndiwo Ataroti-Adara, mpaka Betehoroni wa kumtunda;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa