2 Mbiri 8:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amalinyero ake, ndi anyamata akudziwa za m'nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomoni ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golide, nabwera nao kwa Solomoni mfumu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amalinyero ake, ndi anyamata akudziwa za m'nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomoni ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golide, nabwera nao kwa Solomoni mfumu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Tsono mfumu Hiramu adamtumizira zombo ndi anyamata ake amene ankadziŵa za zapanyanja. Anthuwo adapita ku Ofiri, pamodzi ndi anyamata a Solomoni, ndipo adakatengako golide wa makilogramu 18,000, nabwera naye kwa mfumu Solomoni. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Ndipo Hiramu anatumiza sitima zapamadzi zoyendetsedwa ndi antchito ake, antchito amene ankayidziwa bwino nyanja. Awa pamodzi ndi anthu a Solomoni, anayenda pa madzi kupita ku Ofiri ndipo anakatengako golide olemera makilogalamu 18,000 amene anabwera naye kwa mfumu Solomoni. Onani mutuwo |