Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 8:16 - Buku Lopatulika

16 Momwemo ntchito yonse ya Solomoni inakonzekeratu tsiku lakuika maziko a nyumba ya Yehova, mpaka anaitsiriza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Momwemo ntchito yonse ya Solomoni inakonzekeratu tsiku lakuika maziko a nyumba ya Yehova, mpaka anaitsiriza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Motero ntchito zonse za Solomoni zidatha, kuyambira pamene maziko a Nyumba ya Chauta adaikidwa mpaka pamene ntchitoyo idatha. Choncho Nyumba ya Chauta idatheratu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ntchito yonse ya Solomoni inachitika kuyambira tsiku limene maziko a Nyumba ya Mulungu anakhazikitsidwa mpaka kumaliza. Kotero Nyumba ya Yehova inamalizidwa.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 8:16
6 Mawu Ofanana  

Ndipo omanga nyumba a Solomoni ndi omanga nyumba a Hiramu ndi anthu a ku Gebala anaisema, naikonza mitengo ndi miyala yakumangira nyumbayo.


Maziko ake a nyumba ya Yehova anaikidwa m'chaka chachinai m'mwezi wa Zivi.


Ndipo m'chaka chakhumi ndi chimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.


Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveke kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena chipangizo chachitsulo, pomangidwa iyo.


Ndipo sanapatuke pa lamulo la mfumu la kwa ansembe ndi Alevi, kunena za kanthu kalikonse, kapena za chumachi.


Pamenepo Solomoni anamuka ku Eziyoni-Gebere, ndi ku Eloti m'mphepete mwa nyanja, m'dziko la Edomu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa