2 Mbiri 8:12 - Buku Lopatulika12 Pamenepo Solomoni anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova paguwa la nsembe la Yehova, limene adalimanga pakhomo pachipinda cholowera, Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Pamenepo Solomoni anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe la Yehova, limene adalimanga pakhomo pachipinda cholowera, Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Kenaka Solomoni adapereka nsembe zopsereza kwa Chauta pa guwa la Chauta limene adalimanga patsogolo pa khonde lapoloŵera, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Solomoni anapereka nsembe zopsereza pa guwa lansembe la Yehova limene anamanga patsogolo pa khonde la polowera, Onani mutuwo |
Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.