Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 8:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Solomoni anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mzinda wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Solomoni anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mudzi wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Solomoni adatenga mwana wamkazi wa Farao ku mzinda wa Davide, nabwera naye ku nyumba imene adamangira mkaziyo, poti Solomoniyo ankati, “Mkazi wanga asamakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele, chifukwa chakuti malo amene kwafikira Bokosi lachipangano la Chauta ngopatulika.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Solomoni anabweretsa mwana wamkazi wa Farao mu mzinda wa Davide ku nyumba yaufumu yomwe anamumangira, pakuti iye anati, “Mkazi wanga asakhale mʼnyumba yaufumu ya Davide mfumu ya Israeli, chifukwa malo amene Bokosi la Chipangano la Yehova lafikira ndi opatulika.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 8:11
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumzinda wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.


Ndipo nyumba yake yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khondelo, linamangidwa chimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomoni, yofanafana ndi khonde limeneli.


Koma mwana wamkazi wa Farao anatuluka m'mzinda wa Davide kukwera kunyumba yake adammangira Solomoni, pamenepo iye anamanganso Milo.


Amenewa anali akulu a akapitao a mfumu Solomoni, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu akulamulira anthu.


Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.


Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.


Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Yerusalemu, nuwabenthulire mau malo opatulikawa, nunenere dziko la Israele kulitsutsa;


ndipo mau awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m'phiri lopatulika lija.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa