Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 7:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo Solomoni anapatula pakati pake pa bwalo lili pakhomo pa nyumba ya Yehova; pakuti anapereka nsembe zopsereza, ndi mafuta a nsembe zoyamika pomwepo; popeza guwa la nsembe lamkuwa adalipanga Solomoni linachepa kulandira nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Solomoni anapatula pakati pake pa bwalo lili pakhomo pa nyumba ya Yehova; pakuti anapereka nsembe zopsereza, ndi mafuta a nsembe zoyamika pomwepo; popeza guwa la nsembe lamkuwa adalipanga Solomoni linachepa kulandira nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono Solomoni adapatula malo apakatikati a bwalo lija lokhala kumaso kwa Nyumba ya Chauta, ndipo kumeneko adaperekako nsembe zopsereza ndiponso mafuta a nsembe zachiyanjano, chifukwa chakuti pa guwa lamkuŵa limene adapanga Solomoni lija, panalibe malo oti nkukhalapo nsembe zonse zopsereza ndi zopereka za chakudya, pamodzi ndi mafuta omwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Solomoni anapatula malo a pakati pa bwalo kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndipo pamenepo anapereka nsembe zopsereza ndi mafuta, zopereka za chiyanjano, chifukwa guwa lansembe lamkuwa limene anapanga panalibe malo woti nʼkuperekerapo nsembe zopsereza, nsembe za ufa ndi mafuta.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 7:7
6 Mawu Ofanana  

Ndiponso ansembe aakulu onse ndi anthu anachulukitsa zolakwa zao, monga mwa zonyansa zonse za amitundu, nadetsa nyumba ya Yehova, imene anapatula mu Yerusalemu.


Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono khumi.


Izi muzikonzera Yehova mu zikondwerero zanu zoikika, pamodzi ndi zowinda zanu, ndi zopereka zanu zaufulu, za nsembe zanu zopsereza, ndi za nsembe zanu zaufa, ndi za nsembe zanu zothira, ndi za nsembe zanu zoyamika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa