2 Mbiri 7:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ya ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi makumi awiri. Momwemo mfumu ndi anthu onse anapereka nyumba ya Mulungu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ya ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi makumi awiri. Momwemo mfumu ndi anthu onse anapereka nyumba ya Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Mfumu Solomoni adapereka nsembe pakupha ng'ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000. Motero mfumuyo pamodzi ndi anthu onsewo adaipereka Nyumba ya Mulungu ija. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Kotero mfumu ndi anthu onse anachita mwambo wopereka Nyumba kwa Mulungu. Onani mutuwo |
Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.
Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.