2 Mbiri 7:22 - Buku Lopatulika22 Ndipo adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wa makolo ao amene anawatulutsa m'dziko la Ejipito, nagwira milungu ina, nailambira ndi kuitumikira; chifukwa chake anawagwetsera choipa ichi chonse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Ndipo adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wa makolo ao amene anawatulutsa m'dziko la Ejipito, nagwira milungu ina, nailambira ndi kuitumikira; chifukwa chake anawagwetsera choipa ichi chonse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Tsono azidzati, ‘Nchifukwa chakuti anthuwo adasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao, amene adaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, ndipo adadzifunira milungu ina, namaipembedza ndi kumaitumikira. Nkuwona Chautayo waŵachita zoipa zonsezi.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Anthu adzayankha kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti asiya Yehova, Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto ndipo akangamira milungu ina ndi kumayipembedza ndi kuyitumikira. Choncho Iye wabweretsa zovuta zonsezi.’ ” Onani mutuwo |