17 “Kunena za iwe, ukayenda pamaso panga mokhulupirika monga momwe anachitira abambo ako Davide, ndi kuchita zonse zimene ndakulamula, ndi kusamalitsa malangizo ndi malamulo anga,
nusunge chilangizo cha Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zake, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wake, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, kuti ukachite mwa nzeru m'zonse ukachitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako;
Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga chimene chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wachifumu wa Israele; komatu ana ako achenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.
Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.
Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo.
Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.