Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 7:16 - Buku Lopatulika

16 Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba iyi, kuti dzina langa likhaleko chikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba iyi, kuti dzina langa likhaleko chikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Chifukwa tsopano ndaisankha ndipo ndapatula Nyumba ino kuti dzina langa lizikhala m'menemo mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga, zidzakhala m'menemo nthaŵi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ine ndasankha ndipo ndapatula Nyumba yangayi kotero kuti ndidzakhala mʼmenemo kwamuyaya. Maso ndi mtima wanga zidzakhala pano nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 7:16
22 Mawu Ofanana  

Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga Aisraele m'dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse mwa mafuko onse a Israele kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisraele.


Pamene kumwamba kwatsekera, ndipo kulibe mvula chifukwa cha kuchimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu;


Akatuluka anthu anu kukayambana nkhondo ndi adani ao, kumene konse Inu mudzawatuma, ndipo akapemphera kwa Yehova molunjika kumzinda uno munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;


ndipo akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, m'dziko la adani ao adawatenga ndendewo, ndipo akapemphera kwa Inu molunjika ku dziko lao munapatsa makolo aolo, kumzinda munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;


Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.


Namanga iye maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, Mu Yerusalemu ndidzaika dzina langa.


Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m'malo ake opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kwa inu.


kuti maso anu atsegukire nyumba iyi usana ndi usiku, malo amene munanenerako kuti mudzaikako dzina lanu, kuti mumvere pemphero limene kapolo wanu adzapempha kuloza konkuno.


Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomoni usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe.


Tsopano maso anga adzakhala otsegukira, ndi makutu anga otchera, pemphero la m'malo ano.


Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga monga umo anayendera Davide atate wako, nukachita monga mwa zonse ndakulamulira iwe, nukasunga malemba anga ndi maweruzo anga;


pakuti Yehova anasankha Ziyoni; analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti,


Pampumulo panga mpano posatha, Pano ndidzakhala; pakuti ndakhumbapo.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?


ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


Malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuikako dzina lake akakutanimphirani, muziphako ng'ombe zanu ndi nkhosa ndi mbuzi zanu zimene Yehova anakupatsani, monga ndinakuuzani, ndi kuzidya m'mudzi mwanu, monga umo monse ukhumba moyo wanu.


Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.


pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa