Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 7:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomoni usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomoni usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsono Chauta adamuwonekera usiku namuuza kuti, “Ndamva pemphero lako, ndipo ndadzisankhira malo ano kuti akhale Nyumba yoperekera nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Yehova anamuonekera usiku ndipo anati: “Ine ndamva pemphero lako ndipo ndadzisankhira malo ano kukhala Nyumba yanga yoperekeramo nsembe.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 7:12
17 Mawu Ofanana  

Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Yehova anaonekera kwa Solomoni nthawi yachiwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibiyoni.


Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordani. Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.


Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Ndipo anaika chifanizo chosema chimene adachipanga m'nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomoni mwana wake kuti, M'nyumba muno ndi mu Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israele ndidzaikamo dzina langa kosatha.


Usiku womwewo Mulungu anaonekera kwa Solomoni, nati kwa iye, Pempha chomwe ndikupatse.


Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba iyi, kuti dzina langa likhaleko chikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza.


Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;


Koma Mulungu anamvadi; anamvera mau a pemphero langa.


Pamenepo chopereka cha Yuda ndi Yerusalemu chidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija, ndi ngati zaka zoyamba zija.


Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.


nati Kornelio, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu.


Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa