2 Mbiri 7:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo tsiku la makumi awiri ndi chitatu la mwezi wachisanu ndi chiwiri anawauza anthu apite ku mahema ao, akusekera ndi kukondwera m'mtima mwao chifukwa cha zokoma Yehova adawachitira Davide, ndi Solomoni, ndi Aisraele anthu ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo tsiku la makumi awiri ndi chitatu la mwezi wachisanu ndi chiwiri anawauza anthu apite ku mahema ao, akusekera ndi kukondwera m'mtima mwao chifukwa cha zokoma Yehova adawachitira Davide, ndi Solomoni, ndi Aisraele anthu ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiŵiriwo, Solomoni adauza anthu aja kuti apite kwao. Anthuwo anali okondwa ndiponso a mtima wosangalala, chifukwa cha zokoma zimene Chauta adaachitira Davide ndi Solomoni ndiponso Aisraele, anthu ake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Solomoni anawuza anthu aja kuti apite kwawo. Anthu anali achimwemwe ndi okondwa mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira Davide ndi Solomoni ndiponso anthu ake Aisraeli. Onani mutuwo |
Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.