2 Mbiri 6:5 - Buku Lopatulika5 Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga m'dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse m'mafuko onse a Israele, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu aliyense akhale kalonga wa anthu anga Israele; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga m'dziko la Ejipito, sindinasankha mudzi uliwonse m'mafuko onse a Israele, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu aliyense akhale kalonga wa anthu anga Israele; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Paja adaati, ‘Kuyambira tsiku limene ndidatulutsa anthu anga ku Ejipito, sindidasankhepo mzinda pakati pa mafuko onse a Aisraele woti anthu amangemo nyumba m'mene dzina langa lizimvekamo. Ndipo sindidasankhepo munthu woti nkukhala mfumu yomalamulira Aisraele anthu anga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 ‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga ku Igupto, sindinasankhe mzinda wina uliwonse pa fuko lina lililonse la Aisraeli kuti kumeneko andimangire Nyumba kuti ndizikhalamo kapena munthu wina aliyense kuti akhale mtsogoleri wa Aisraeli anthu anga. Onani mutuwo |
Nadzilimbitsa Rehobowamu mfumu mu Yerusalemu, nachita ufumu; pakuti Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri mu Yerusalemu, ndiwo mzinda Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele, kuikapo dzina lake; ndipo dzina la make ndiye Naama Mwamoni.