Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 6:4 - Buku Lopatulika

4 Nati iye, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, wakunena m'kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi manja ake, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Nati iye, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, wakunena m'kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi manja ake, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndipo mfumuyo idati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene wachitadi ndi dzanja lake zimene adaalonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide bambo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo inati, “Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli amene wachita ndi dzanja lake zimene analonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide abambo anga. Pakuti Iye anati,

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 6:4
17 Mawu Ofanana  

Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israele amene analankhula m'kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lake, nati,


Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wake kosatha.


Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.


Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.


inu amene mwasungira mtumiki wanu Davide atate wanga chija mudamlonjezachi: inde munanena ndi pakamwa panu, ndipo mwachita ndi dzanja lanu, monga momwe muli lero lino.


Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, achitike mau anu amene munanena kwa Davide mtumiki wanu.


Ndipo mfumu inapotolokera nkhope yake, nidalitsa khamu lonse la Israele; ndi khamu lonse la Israele linaimirira.


Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga m'dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse m'mafuko onse a Israele, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu aliyense akhale kalonga wa anthu anga Israele;


Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkulu. Navomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi.


Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen.


Imbirani Mulungu, liimbireni nyimbo dzina lake; undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha; dzina lake ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.


Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.


Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa