Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 6:34 - Buku Lopatulika

34 Akatulukira kunkhondo anthu anu kuyambana ndi adani ao, kutsata njira iliyonse muwatumiza; nakapemphera kwa Inu kuloza kumzinda uwu munausankha, ndi nyumba iyi ndaimangira dzina lanu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Akatulukira kunkhondo anthu anu kuyambana ndi adani ao, kutsata njira iliyonse muwatumiza; nakapemphera kwa Inu kuloza kumudzi uwu munausankha, ndi nyumba iyi ndaimangira dzina lanu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 “Anthu anu akamapita ku nkhondo kukamenyana ndi adani ao, kulikonse kumene mungaŵatume, akapemphera kwa Inu choyang'ana ku mzinda uno umene Inu mudausankha, ndiponso ku Nyumba imene ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 “Anthu akapita ku nkhondo kukamenyana ndi adani awo, kulikonse kumene mungawatume, ndipo akapemphera moyangʼana mzinda uno umene mwausankha ndi Nyumba yanu imene ndakumangirani,

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 6:34
19 Mawu Ofanana  

Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo Inu nthawi zosatha.


Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israele. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anafuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapatukitsa amleke.


Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anachokera kumizinda yonse ya Yuda kufuna Yehova.


pamenepo mumvere Inu mu Mwamba mokhala Inumo, nimumchitire mlendoyo monga mwa zonse akuitanirani; kuti mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi adziwe dzina lanu, nakuopeni, monga amatero anthu anu Aisraele; ndi kuti adziwe kuti nyumba iyi ndamangayi itchedwa ndi dzina lanu.


pamenepo mumvere mu Mwamba pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.


Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.


Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira.


Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.


Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konsekonse Aamaleke akuchita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha.


Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa