Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 6:2 - Buku Lopatulika

2 Koma ndakumangirani nyumba yokhalamo, malo okhazikika okhalamo Inu nthawi yosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Koma ndakumangirani nyumba yokhalamo, malo okhazikika okhalamo Inu nthawi yosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndiye ine ndakumangirani nyumba yaulemerero, malo oti muzikhalamo nthaŵi zonse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ine ndakumangirani Nyumba yokongola kwambiri, malo woti muzikhalamo mpaka muyaya.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 6:2
19 Mawu Ofanana  

Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wake ku nthawi zonse.


Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo Inu nthawi zosatha.


Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wake kosatha.


Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Limbika, nulimbe mtima, nuchichite; usaopa, kapena kutenga nkhawa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusowa kapena kukutaya mpaka zitatha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova.


Ndipo anati kwa ine, Solomoni mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wake.


Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kuchokera ku Kiriyati-Yearimu kunka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema ku Yerusalemu.


Pamenepo Solomoni anati, Yehova anati kuti adzakhala mu mdima wandiweyani.


Ndipo mfumu inapotolokera nkhope yake, nidalitsa khamu lonse la Israele; ndi khamu lonse la Israele linaimirira.


ndi kumuka nazo siliva ndi golide, zimene mfumu ndi aphungu ake, anapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Israele, mokhala mwake muli mu Yerusalemu,


pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu;


kufikira nditapezera Yehova malo, chokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?


Alemekezedwe Yehova kuchokera mu Ziyoni, amene akhala mu Yerusalemu. Aleluya.


Kalongayo tsono, polowa iwo alowe pakati pao, ndipo potuluka iwo atulukire pamodzi.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa