Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 6:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Solomoni anaima ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasula manja ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Solomoni anaima ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasula manja ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pambuyo pake Solomoni adaimirira patsogolo pa guwa la Chauta, msonkhano wonse wa Aisraele akuwona, ndipo adatambalitsa manja ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pamenepo Solomoni anayimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova patsogolo pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 6:12
15 Mawu Ofanana  

napenya, ndipo taonani, mfumu ili chilili pachiundo, monga ankachita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfumu; nakondwerera anthu onse a m'dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nafuula Chiwembu, Chiwembu.


Niima mfumu pachiunda, ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a chipangano cholembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli.


Ndipo ndalongamo likasa, muli chipangano cha Yehova, anachichita ndi ana a Israele.


Ndipo Solomoni adapanga chiunda chamkuwa, m'litali mwake mikono isanu, ndi msinkhu wake mikono itatu, nachiika pakati pa bwalo; ndipo anaima pamenepo nagwada pa maondo ake pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasulira manja ake kumwamba;


Ukakonzeratu mtima wako, ndi kumtambasulira Iye manja ako;


Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.


Nditambalitsira manja anga kwa Inu: Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.


Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.


Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.


Akulu adzafumira ku Ejipito; Kusi adzafulumira kutambalitsa manja ake kwa Mulungu.


Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m'mzinda nakweza manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko.


Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.


Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa