Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 6:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo ndalongamo likasa, muli chipangano cha Yehova, anachichita ndi ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo ndalongamo likasa, muli chipangano cha Yehova, anachichita ndi ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono m'menemo ndaikamo Bokosi lija m'mene muli mau a chipangano cha Chauta chimene adachita ndi Aisraele.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Mʼmenemo ndayikamo Bokosi la Chipangano, mmene muli pangano la Yehova limene anapangana ndi ana a Israeli.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 6:11
9 Mawu Ofanana  

Ndipo ndakonzera malo likasalo, m'mene muli chipangano cha Yehova, chimene anapangana ndi makolo athu pamene anawatulutsa m'dziko la Ejipito.


Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja a mwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israele, potuluka iwo m'dziko la Ejipito.


Munalibe kanthu kena m'likasa, koma magome awiri Mose anawaika m'mwemo ku Horebu, muja Yehova anachita chipangano ndi ana a Israele potuluka iwo mu Ejipito.


Ndipo ansembe analowa nalo likasa la chipangano la Yehova kumalo kwake m'chipinda chamkati mwa Kachisi, m'malo opatulika kwambiri, pansi pa mapiko a akerubi.


Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake adanenawo, pakuti ndinauka ine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga analonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumbayi.


Ndipo Solomoni anaima ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasula manja ake.


Mundisonkhanitsire okondedwa anga, amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.


Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;


okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa