Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 6:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake adanenawo, pakuti ndinauka ine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga analonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumbayi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake adanenawo, pakuti ndinauka ine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga analonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumbayi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsopano Chauta wachitadi zimene adaalonjeza zija. Pakuti ine ndi amene ndaloŵa ufumu m'malo mwa Davide bambo wanga, ndipo ndikulamulira Aisraele pa mpando wa bambo wanga, monga momwe Chauta adaalonjezera. Ndipo ndinedi amene ndamanga Nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Yehova wasunga zimene analonjeza. Ine ndalowa mʼmalo mwa abambo anga Davide, ndipo tsopano ndili pa mpando waufumu wa Israeli, monga momwe Yehova analonjezera, ndipo ndamangira nyumba Dzina la Yehova Mulungu wa Israeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 6:10
12 Mawu Ofanana  

Tsono Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo ufumu wake unakhazikika kwakukulu.


Ndipo kudzachitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.


Tsono, mwana wanga, Yehova akhale nawe; nulemerere, numange nyumba ya Yehova Mulungu wako monga ananena za iwe.


ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana aamuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele.


Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.


Momwemo Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Yehova, ndiye mfumu m'malo mwa Davide atate wake, nalemerera, namvera iye Aisraele onse.


Ndipo Solomoni mwana wa Davide analimbikitsidwa mu ufumu wake, ndipo Yehova Mulungu wake anali naye, namkuza kwakukulu.


Ndipo ndalongamo likasa, muli chipangano cha Yehova, anachichita ndi ana a Israele.


koma sudzandimangira nyumba ndiwe, koma mwana wako wakudzatuluka m'chuuno mwako, iyeyo adzalimangira dzina langa nyumbayi.


Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa