Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 5:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo ansembe analowa nalo likasa la chipangano la Yehova kumalo kwake m'chipinda chamkati mwa Kachisi, m'malo opatulika kwambiri, pansi pa mapiko a akerubi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo ansembe analowa nalo likasa la chipangano la Yehova kumalo kwake m'chipinda chamkati mwa Kachisi, m'malo opatulika kwambiri, pansi pa mapiko a akerubi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono ansembe adafika nalo Bokosi lachipangano la Chauta lija ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana naliika kunsi kwa mapiko a akerubi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ansembe anafika nalo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼchipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndipo analiyika pansi pa mapiko a Akerubi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 5:7
13 Mawu Ofanana  

Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la chipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, kunyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.


Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisraele onse, ndiwo opatulikira Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ake Israele.


ndi zoikaponyali ndi nyali zake za golide woona, zakuunikira monga mwa chilangizo chake chakuno cha chipinda chamkati;


Nadza akuluakulu onse a Israele, nanyamula likasalo Alevi.


Ndi mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kuchuluka kwake.


Pakuti akerubi anafunyulula mapiko ao pamalo a likasa, ndi akerubi anaphimba likasa ndi mphiko zake pamwamba pake.


Ndipo ndalongamo likasa, muli chipangano cha Yehova, anachichita ndi ana a Israele.


Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu; Inu ndi hema wa mphamvu yanu.


Anayesanso m'kati mwa Kachisi m'tsogolomo, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; ndipo anati kwa ine, Umo m'mopatulika kwambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa