Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 5:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo anakwera nalo likasa, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika zinali m'chihemamo; izizo ansembe Alevi anakwera nazo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anakwera nalo likasa, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika zinali m'chihemamo; izizo ansembe Alevi anakwera nazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adabwera nalo Bokosilo pamodzi ndi chihema chamsonkhano ndiponso ziŵiya zonse zopatulika zimene zinali m'chihemamo. Ansembe ndi Alevi ndiwo amene adabwera nazo zimenezo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 ndipo anabwera nalo bokosi lija pamodzi ndi tenti ya msonkhano ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali mʼmenemo. Ansembe ndi Alevi ndiye anazinyamula,

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 5:5
6 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'chihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.


Ndipo ansembe analonga likasa la chipangano cha Yehova kumalo kwake, ku chipinda chamkati, ku malo opatulika kwambiri, munsi mwa mapiko a akerubi.


Ndipo Solomoni ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibiyoni; pakuti kumeneko kunali chihema chokomanako cha Mulungu adachimanga Mose mtumiki wa Yehova m'chipululu.


Ndipo Yehoyada anaika mayang'aniro a nyumba ya Yehova m'dzanja la ansembe Aleviwo, amene Davide anawagawa, ayang'anire nyumba ya Yehova; napereka nsembe zopsereza za Yehova monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, ndi kukondwera ndi kuimbira, monga mwa chilangizo cha Davide.


Nadza akuluakulu onse a Israele, nanyamula likasalo Alevi.


Ndi mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kuchuluka kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa