Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 5:12 - Buku Lopatulika

12 Alevi omwe akuimba, onsewo ndiwo Asafu, Hemani, Yedutuni, ndi ana ao, ndi abale ao ovala bafuta, ali nazo nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, anaima kum'mawa kwa guwa la nsembe, ndi pamodzi nao ansembe zana limodzi mphambu makumi awiri akuomba malipenga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Alevi omwe akuimba, onsewo ndiwo Asafu, Hemani, Yedutuni, ndi ana ao, ndi abale ao ovala bafuta, ali nazo nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, anaima kum'mawa kwa guwa la nsembe, ndi pamodzi nao ansembe zana limodzi mphambu makumi awiri akuomba malipenga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pamenepo Alevi onse amene ankaimba nyimbo, Asafu, Hemani ndi Yedutuni, ana ao pamodzi ndi abale ao, ovala nsalu za bafuta wambee, ali ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe, adaimirira cha kuvuma kwa guwa, pamodzi ndi ansembe okwanira 120 amene ankaimba malipenga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Alevi onse amene anali oyimba: Asafu, Hemani, Yedutuni ndi ana ndiponso abale awo, amayima mbali ya kummawa kwa guwa lansembe atavala zovala zofewa zosalala akuyimba ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe. Ansembe onse amene amayimba malipenga analipo 120 pamodzi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 5:12
26 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ndi Aisraele onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga.


Ndi Sebaniya, ndi Yosafati, ndi Netanele, ndi Amasai, ndi Zekariya, ndi Benaya, ndi Eliyezere, ansembe, analiza malipenga ku likasa la Mulungu; ndi Obededomu ndi Yehiya anali odikira a likasa.


Ndipo Davide anavala malaya abafuta, ndi Alevi onse akunyamula likasa, ndi oimba, ndi Kenaniya woyang'anira kusenzaku, pamodzi ndi oimba; Davide anavalanso efodi wabafuta.


ndi kuimirira m'mawa ndi m'mawa kuyamika ndi kulemekeza Yehova, momwemonso madzulo;


ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo.


Ndipo oimirirawo, ndi ana ao, ndi awa: a ana a Akohati, Hemani woimbayo, mwana wa Yowele, mwana wa Samuele,


Ndi mbale wake Asafu wokhala ku dzanja lake lamanja, ndiye Asafu mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,


Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ake.


Alevi tsono anaimirira ndi zoimbira za Davide, ndi ansembe anakhala ndi malipenga.


Naimirira ansembe mu udikiro wao; ndi Alevi omwe ndi zoimbira za Yehova, adazipanga Davide mfumu kuyamika nazo Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire, polemekeza Davide mwa utumiki wao; ndi ansembe anaomba malipenga pamaso pao, nakhala chilili Israele yense.


Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.


Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.


Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye.


Oimbira anatsogolera, oimba zoimba anatsata m'mbuyo, pakatipo anamwali oimba mangaka.


Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa, ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.


Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa; pazeze ndi kulira kwake.


ndipo anatuluka mu Kachisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atavala malaya woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolide pachifuwa pao.


Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbuu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa