Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 5:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo ansembe anatuluka m'malo opatulika, pakuti ansembe onse anali komwe adadzipatula, osasunga magawidwe ao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo ansembe anatuluka m'malo opatulika, pakuti ansembe onse anali komwe adadzipatula, osasunga magawidwe ao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono ansembe adatulukamo m'malo opatulikawo (poti ansembe onse amene analipo anali atadziyeretsa, osayang'aniranso magulu ao.)

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Kenaka ansembe anatulukamo mʼMalo Opatulika. Ansembe onse amene anali mʼmenemo anali atadziyeretsa posayangʼaniranso magulu awo ochokera.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 5:11
13 Mawu Ofanana  

Momwemo ansembe ndi Alevi anadzipatula kuti akwere nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele.


Ndipo anamemeza abale ao, nadzipatula, nalowa monga adawauza mfumu mwa mau a Yehova, kuyeretsa nyumba ya Yehova.


Koma ansembe anaperewera, osakhoza kusenda nsembe zonse zopsereza; m'mwemo abale ao Alevi anawathandiza, mpaka idatha ntchitoyi, mpaka ansembe adadzipatula; pakuti Alevi anaposa ansembe m'kuongoka mtima kwao kudzipatula.


nanena nao, Ndimvereni, Alevi inu, dzipatuleni, nimupatule nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu, ndi kuchotsa zoipsa m'malo opatulika.


Pamenepo anaphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wachiwiri, ndipo ansembe ndi Alevi anachita manyazi, nadzipatula, nabwera nazo nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova.


Ndipo mudzikonzere monga mwa nyumba za makolo anu, m'zigawo zanu, monga umo adalembera Davide mfumu ya Israele, ndi umo adalembera Solomoni mwana wake.


Ndipo muphere Paska, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kuchita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.


Alevi omwe akuimba, onsewo ndiwo Asafu, Hemani, Yedutuni, ndi ana ao, ndi abale ao ovala bafuta, ali nazo nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, anaima kum'mawa kwa guwa la nsembe, ndi pamodzi nao ansembe zana limodzi mphambu makumi awiri akuomba malipenga.


Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m'mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa