Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 5:10 - Buku Lopatulika

10 Munalibe kanthu kena m'likasa, koma magome awiri Mose anawaika m'mwemo ku Horebu, muja Yehova anachita chipangano ndi ana a Israele potuluka iwo mu Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Munalibe kanthu kena m'likasa, koma magome awiri Mose anawaika m'mwemo ku Horebu, muja Yehova anachita chipangano ndi ana a Israele potuluka iwo m'Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 M'Bokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iŵiri yokha ija imene Mose adaaikamo ku Horebu, kumene Chauta adaachita chipangano ndi Aisraele, iwowo atatuluka ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mʼbokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iwiri imene Mose anayikamo ku Horebu, kumene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 5:10
14 Mawu Ofanana  

Ndipo ndalongamo likasa, muli chipangano cha Yehova, anachichita ndi ana a Israele.


Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;


Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.


Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mau omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa.


Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;


Awa ndi mau a chipangano chimene Yehova analamulira Mose achichite ndi ana a Israele m'dziko la Mowabu, pamodzi ndi chipanganocho anachita nao mu Horebu.


okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa