Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 4:22 - Buku Lopatulika

22 ndi zozimira nyali, ndi mbale zowazira, ndi zipande, ndi mbale za zofukiza za golide woona; ndi kunena za polowera m'nyumba, zitseko zake za m'katimo za malo opatulika kwambiri, ndi zitseko za nyumbayi, ndiyo Kachisi, zinali zagolide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 ndi zozimira nyali, ndi mbale zowazira, ndi zipande, ndi mbale za zofukiza za golide woona; ndi kunena za polowera m'nyumba, zitseko zake za m'katimo za malo opatulika kwambiri, ndi zitseko za nyumbayi, ndiyo Kachisi, zinali zagolide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Zozimira nyale, mabeseni, mbale zofukiziramo lubani ndiponso ziwaya zopalira moto, zonsezi za golide weniweni. Ndipo adapangitsa zomangira zitseko za Nyumba ya Chauta ija, zitseko zam'kati zoloŵera ku malo opatulika kopambana, ndiponso zitseko zoloŵera m'Nyumba ya Chauta, zonsezo zinali zagolide.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 zozimitsira nyale zagolide weniweni, mbale zowazira magazi, mbale ndi zofukizira; ndiponso zitseko zagolide za Nyumba ya Mulungu, chitseko cha ku Malo Opatulika Kwambiri ndi zitseko za ku chipinda chachikulu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 4:22
12 Mawu Ofanana  

Ndipo analembapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, nakuta zolembazo ndi golide wopsapsala.


ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira moto za golide woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolide, za zitseko za chipinda cha m'katimo, malo opatulika kwambiri, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kachisi.


Koma sanapangire nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera zilizonse zagolide, kapena zotengera zilizonse zasiliva, kuzipanga ndi ndalama adabwera nazo kunyumba ya Yehova;


Nachotsanso miphika, ndi zoolera, ndi zozimira nyali, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo.


ndi maluwa, ndi nyali, ndi mbano zagolide, ndiwo golide wangwiro;


Momwemo zidatha ntchito zonse Solomoni adazichitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni anabwera nazo zopatulika zija za atate wake Davide; naziika siliva, ndi golide, ndi zipangizo zonse m'chuma cha nyumba ya Mulungu.


Ndipo mbano zake, ndi zoolera zake, zikhale za golide woona.


Ndipo uzipanga zotayira zake zakulandira mapulusa ake, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake, ndi mitungo yake, ndi zopalira moto zake; zipangizo zake zonse uzipanga zamkuwa.


Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziwiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golide woona.


Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazichotsa.


Ndipo pamakomopo panali zitseko zopatukana zotembenuzika, china chopatukana pa khomo lina china pa linzake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa