Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 4:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo Solomoni anazipanga zipangizo izi zonse zochulukadi, pakuti kulemera kwake kwa mkuwa sikunayeseke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo Solomoni anazipanga zipangizo izi zonse zochulukadi, pakuti kulemera kwake kwa mkuwa sikunayeseka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Solomoni adapangitsa zinthu zimenezo zochuluka kwambiri, kotero kuti kulemera kwa mkuŵawo sikudadziŵike ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Zinthu zonse zimene Solomoni anapanga zinali zochuluka kwambiri kotero kuti kulemera kwa mkuwa sikunadziwike.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 4:18
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinachuluka ndithu; kulemera kwake kwa mkuwa wonsewo sikunayeseke.


Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golide, ndi matalente zikwizikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, osayesa kulemera kwake, pakuti zidachulukadi; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.


Nakonzeratu Davide chitsulo chochuluka cha misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wochuluka wosauyesa kulemera kwake;


Mfumuyi inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zereda.


Nsanamira ziwirizo, thawale limodzilo, ndi ng'ombe zamkuwa zinali pansi pa zoikapo, zimene mfumu Solomoni anazipangira nyumba ya Yehova; mkuwa wa zipangizo zonsezi sanathe kuyesa kulemera kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa