Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 4:16 - Buku Lopatulika

16 Miphika yomwe, ndi zoolera, ndi mitungo, ndi zipangizo zake zonse, Huramuabi anazipangira mfumu Solomoni, kuzipangira nyumba ya Yehova, za mkuwa wonyezimira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Miphika yomwe, ndi zoolera, ndi mitungo, ndi zipangizo zake zonse, Huramuabi anazipangira mfumu Solomoni, kuzipangira nyumba ya Yehova, za mkuwa wonyezimira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Mikhate, mafosholo, mafoloko ndiponso zipangizo zonse zofunikira pa zimenezi, Huramuabi adazipanga za mkuŵa wonyezemira, kupangira mfumu Solomoni ku Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Miphika, mafosholo, mafoloko otengera nyama ndi ziwiya zina zonse. Zipangizo zonse zimene Hiramu Abi anapangira Mfumu Solomoni za mʼNyumba ya Yehova zinali zamkuwa wonyezimira.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 4:16
13 Mawu Ofanana  

ndi miphikayo, ndi zoolerazo, ndi mbalezo; inde zotengera zonse zimene Hiramu anampangira mfumu Solomoni za m'nyumba ya Yehova, zinali za mkuwa wonyezimira.


Nachotsanso miphika, ndi zoolera, ndi zozimira nyali, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo.


Ndi ku Tibati, ndi ku Kuni, mizinda ya Hadadezere, Davide anatenga mkuwa wambiri, ndiwo umene Solomoni anayenga nao thawale lamkuwa, ndi nsanamira, ndi zipangizo zamkuwa.


ndi mitengo, ndi mbale zowazira, ndi zikho za golide woona, ndi cha mitsuko yake yagolide, woyesedwa kulemera kwake mtsuko uliwonse; ndi cha mitsuko yasiliva woyesedwa kulemera kwake mtsuko uliwonse;


Ndipo tsono ndatumiza munthu waluso wokhala nalo luntha, Huramuabi,


Ndipo Huramu anapanga miphika, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake. Natsiriza Huramu ntchito adaichitira mfumu Solomoni m'nyumba ya Mulungu:


thawale limodzi ndi ng'ombe khumi ndi ziwiri pansi pake.


Mfumuyi inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zereda.


Ndipo uzipanga zotayira zake zakulandira mapulusa ake, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake, ndi mitungo yake, ndi zopalira moto zake; zipangizo zake zonse uzipanga zamkuwa.


Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zopalira moto; zipangizo zake zonse anazipanga zamkuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa