9 Pambuyo pake Senakeribu mfumu ya Asiriya, akali ku Lakisi ndi mphamvu yake yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti,
9 Pambuyo pake Senakeribu mfumu ya Asiriya, akali ku Lakisi ndi mphamvu yake yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti,
9 Pambuyo pa zimenezi Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, amene anali atazinga mzinda wa Lakisi pamodzi ndi ankhondo ake onse, adatuma akazembe ake ku Yerusalemu kwa Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi kwa anthu onse a ku Yuda amene anali mu Yerusalemu. Adaŵatuma ndi mau akuti,
9 Nthawi ina, pamene Senakeribu mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo anali atazinga Lakisi, iye anatumiza atsogoleri ake ankhondo ku Yerusalemu ndi uthenga uwu kwa Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a ku Yuda amene anali kumeneko:
Ndipo mfumu ya Asiriya anatuma nduna ndi mkulu wa adindo ndi kazembe ochokera ku Lakisi ndi khamu lalikulu la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima kumcherenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku Malo a Wotsuka Thonje.
Ndipo mfumu ya Asiriya inatumiza kazembe kuchokera pa Lakisi, kunka ku Yerusalemu, kwa mfumu Hezekiya, ndi nkhondo yambiri. Ndipo iye anaima chifupi ndi mcherenje wa thamanda la kumtunda, m'khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu.
Manga galeta kukavalo waliwiro, wokhala mu Lakisi iwe, woyamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni ndi iye; pakuti zolakwa za Israele zinapezedwa mwa iwe.