Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 32:4 - Buku Lopatulika

4 Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati padziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asiriya ndi kupeza madzi ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati pa dziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asiriya ndi kupeza madzi ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 ndipo anthu ambiri adasonkhana kuti atseke akasupe onse pamodzi ndi mfuleni womwe umene unkayenda m'kati mwa nthakamo. Iwo ankati, “Akafika kuno mafumu a ku Asiriya, adzapezerenji madzi ambiri?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Gulu lalikulu la anthu linasonkhana, ndipo anatseka akasupe onse pamodzi ndi mtsinje umene umayenda mʼkati mwa nthakamo. Iwo ankanena kuti, “Nʼchifukwa chiyani mafumu a Asiriya akabwera kuno adzapeze madzi ambiri?”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 32:4
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.


Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?


Chaka chakhumi ndi zinai cha Hezekiya Senakeribu mfumu ya Asiriya anakwerera mizinda yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.


Ndipo kunali chaka chachinai cha mfumu Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele Salimanezere mfumu ya Asiriya anakwerera Samariya, naumangira misasa.


Zoona, Yehova, mafumu a Asiriya anapasula amitundu ndi maiko ao,


Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yake yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mchera, nautengera mzinda madzi, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?


Ndipo anauka nachotsa maguwa a nsembe okhala mu Yerusalemu, nachotsa pofukizira zonunkhira, naziponya m'mtsinje wa Kidroni.


Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Senakeribu mfumu ya Asiriya, nalowera Yuda, namangira mizinda yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi.


anapangana ndi akulu ake ndi amphamvu ake, kutseka madzi a mu akasupe okhala kunja kwa mzinda; namthandiza iwo.


Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire kumadzulo kwa mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo ntchito zake zonse.


Popeza ati, Akalonga anga kodi sali onse mafumu?


Inu munapanganso chosungamo madzi a thamanda lakale, pakati pa malinga awiri; koma inu simunamuyang'ane iye amene anachichita icho, ngakhale kusamalira iye amene analipanga kale.


Ndipo inu munaona kuti pa mzinda wa Davide panagumuka mipata yambiri; ndipo munasonkhanitsa pamodzi madzi a m'thamanda lakunsi.


Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng'anjo yanjerwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa