Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 32:32 - Buku Lopatulika

32 Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi ntchito zake zokoma, taonani, zilembedwa m'masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi ntchito zake zokoma, taonani, zilembedwa m'masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Tsono ntchito zonse za Hezekiya, pamodzi ndi zabwino zimene ankachita, zidalembedwa m'nkhani yosimba za zimene Yesaya mneneri mwana wa Amozi adaziwona m'masomphenya. Nkhani imeneyi idalembedwa m'buku la mafumu a ku Yuda ndi a ku Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Hezekiya ndi ntchito za kudzipereka kwake zalembedwa mʼmasomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 32:32
9 Mawu Ofanana  

Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yake yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mchera, nautengera mzinda madzi, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?


Machitidwe ena tsono a Amaziya, oyamba ndi otsiriza, taonani, sanalembedwe kodi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele?


Machitidwe ena tsono a Uziya, oyamba ndi otsiriza, anawalemba Yesaya mneneri mwana wa Amozi.


Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babiloni, amene anatumiza kwa iye kufunsira za chodabwitsa chija chidachitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwake.


Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ake, namuika polowerera kumanda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala mu Yerusalemu anamchitira ulemu pa imfa yake. Ndipo Manase mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Machitidwe ena tsono a Yosiya, ndi ntchito zake zokoma, monga mulembedwa m'chilamulo cha Yehova,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa