Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 32:3 - Buku Lopatulika

3 anapangana ndi akulu ake ndi amphamvu ake, kutseka madzi a mu akasupe okhala kunja kwa mzinda; namthandiza iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 anapangana ndi akulu ake ndi amphamvu ake, kutseka madzi a m'akasupe okhala kunja kwa mudzi; namthandiza iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 adapangana ndi nduna zake pamodzi ndi atsogoleri a gulu lankhondo, kuti akatseke madzi a ku akasupe kunja kwa mzindawo. Anthuwo adamthandiza,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 iye anakambirana ndi akuluakulu ake pamodzi ndi atsogoleri a gulu lankhondo za kutseka akasupe ochoka ku kasupe amene anali kunja kwa mzinda, ndipo iwo anamuthandiza.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 32:3
13 Mawu Ofanana  

Ukuti koma ndiwo mau a pakamwa pokha, Pali uphungu ndi mphamvu ya kunkhondo. Tsono ukhulupirira yani, kuti undipandukira?


Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yake yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mchera, nautengera mzinda madzi, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?


Pakuti mfumu idapangana ndi akulu ake, ndi msonkhano wonse wa mu Yerusalemu, kuti achite Paska mwezi wachiwiri.


Ndipo pakuona Hezekiya kuti wadza Senakeribu, ndi kuti nkhope yake inalunjikitsa kuyambana nkhondo ndi Yerusalemu,


Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire kumadzulo kwa mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo ntchito zake zonse.


Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati padziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asiriya ndi kupeza madzi ambiri.


Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.


Uphungu utsimikiza zolingalira, ponya nkhondo utapanga upo.


Pakuti udzaponya nkhondo yako ndi upo, ndi kupulumuka pochuluka aphungu.


Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lake, ndi kumphunzitsa Iye?


Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng'anjo yanjerwa.


Pakuti anadziwitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala phungu wake ndani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa