Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 32:13 - Buku Lopatulika

13 Simudziwa kodi chomwe ine ndi makolo anga tachitira anthu onse a m'maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m'dzanja langa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Simudziwa kodi chomwe ine ndi makolo anga tachitira anthu onse a m'maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m'dzanja langa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Kodi inu simukudziŵa zimene ine ndi makolo anga takhala tikuichita mitundu yonse ya anthu a maiko ena? Kodi milungu ya mitundu ina ya anthu a m'maikowo idatha kupulumutsa maiko ao m'manja mwanga?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 “Kodi inu simukudziwa zimene ine ndi makolo anga tachita kwa anthu a mitundu ina? Kodi milungu ya mitundu imeneyi inatha kupulumutsa dziko lawo kuchoka mʼdzanja langa?

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 32:13
20 Mawu Ofanana  

Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


Ndi uti mwa milungu yonse ya mitunduyi ya anthu, amene makolo anga anawaononga konse, unakhoza kulanditsa anthu ake m'dzanja mwanga?


Nanenera Mulungu wa Yerusalemu, monga umo amanenera milungu ya mitundu ya anthu a padziko lapansi, ndiyo ntchito ya manja a anthu.


dzanja langa lapeza monga chisa, chuma cha mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa mazira osiyidwa, ine ndasonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe chogwedeza phiko, kapena chotsegula pakamwa, kapena cholira pyepye.


Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?


Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.


ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.


Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:


Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu padziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa