2 Mbiri 32:12 - Buku Lopatulika12 Sanaichotse misanje yake ndi maguwa ake a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire kuguwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Sanaichotse misanje yake ndi maguwa ake a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire kuguwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Kodi si Hezekiya yemweyu amene adachotsa akachisi ndi maguwa ku mapiri, nalamula anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu kuti, “Muzipembedza ku guwa limodzi lokha ndipo muzipereka nsembe zanu zopsereza pa guwa limodzi lokhalo?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Kodi si Hezekiya amene anachotsa malo opembedzerapo Mulungu ameneyu ndi maguwa ansembe ndi kunena kwa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe limodzi ndi kupserezapo nsembe?’ Onani mutuwo |
Chitatha ichi chonse tsono, Aisraele onse opezekako anatuluka kunka kumizinda ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe mu Yuda monse, ndi mu Benjamini, mu Efuremunso, ndi mu Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israele anabwerera, yense kudziko lake ndi kumizinda yao.