2 Mbiri 32:1 - Buku Lopatulika1 Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Senakeribu mfumu ya Asiriya, nalowera Yuda, namangira mizinda yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Senakeribu mfumu ya Asiriya, nalowera Yuda, namangira midzi yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pambuyo pake, zitatha ntchito zachikhulupirirozi, Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, adabwera kudzathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo adamanga zithando zankhondo kuzinga mizinda yamalinga. Ankati aŵagumule malinga akewo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Zitatha zonse zimene Hezekiya anachita mokhulupirika, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anabwera ndi kuthira nkhondo dziko la Yuda. Iye anazinga mizinda yotetezedwa ya Yuda, kuganiza kuti ayigonjetsa. Onani mutuwo |