Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 30:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israele ndi Yuda onse, nalembanso makalata kwa Efuremu ndi Manase, kuti abwere kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israele ndi Yuda onse, nalembanso akalata kwa Efuremu ndi Manase, kuti abwere kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Hezekiya adatumiza mau ku Israele konse ndi ku Yuda, ndipo adalembanso makalata kwa Aefuremu ndi kwa Amanase kuti, “Mubwere ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, kudzachita mwambo wa Paska ya Chauta, Mulungu wa Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Hezekiya anatumiza uthenga mʼdziko lonse la Israeli ndi ku Yuda ndiponso analemba makalata ku Efereimu ndi Manase, oyitana anthu kuti abwere ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 30:1
17 Mawu Ofanana  

Zedi silinachitike Paska lotere chiyambire masiku a oweruza anaweruza Israele, ngakhale m'masiku a mafumu a Israele, kapena mafumu a Yuda;


Ndipo ansembe ndi Alevi okhala mu Israele yense anadziphatikiza kwa iye, ochokera m'malire ao onse.


Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m'mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.


Koma anamdzera munthu wa Mulungu, kuti, Mfumu, khamu la nkhondo la Israele lisapite nanu; pakuti Yehova sakhala ndi Israele, sakhala ndi ana onse a Efuremu.


ndi ansembewo anawapha, nachita nsembe yauchimo ndi mwazi wao paguwa la nsembe, kuchita chotetezera Aisraele onse; pakuti mfumu idauza kuti nsembe yopsereza ndi nsembe yauchimo zikhale za Aisraele onse.


Nakondwera Hezekiya ndi anthu onse pa ichi Mulungu adakonzeratu; pakuti chinthuchi chidachitika modzidzimutsa.


Pakuti mfumu idapangana ndi akulu ake, ndi msonkhano wonse wa mu Yerusalemu, kuti achite Paska mwezi wachiwiri.


Ndipo muphere Paska, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kuchita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.


Amenewa ndi mau a kalata ija anatumiza Yeremiya mneneri kuchokera ku Yerusalemu kunka kwa akulu otsala a m'nsinga, ndi kwa ansembe, ndi kwa aneneri, ndi kwa anthu onse, amene Nebukadinezara anawatenga ndende ku Yerusalemu kunka ku Babiloni;


Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.


Machitidwe ao sawalola kubwerera kwa Mulungu wao; pakuti mzimu wa uhule uli m'kati mwao, ndipo sadziwa Yehova.


Pakuti ana a Yosefe ndiwo mafuko awiri, Manase ndi Efuremu; ndipo sanawagawire Alevi kanthu m'dziko, koma mizinda yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi chuma chao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa