2 Mbiri 3:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo anamanga malo opatulika kwambiri, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; naikuta ndi golide wabwino wakufikira matalente mazana asanu ndi limodzi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo anamanga malo opatulika kwambiri, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; naikuta ndi golide wabwino wakufikira matalente mazana asanu ndi limodzi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Kenaka adapanga malo opatulika kwambiri. M'litali mwake anali a mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwa nyumbayo. M'mimba mwake analinso a mamita asanu ndi anai. Adakuta malo opatulikawo ndi golide wosalala wokwanira matani makumi aŵiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Iye anamanga Malo Opatulika Kwambiri ndipo mulitali mwake munali mofanana ndi mulifupi mwa Nyumba mamita asanu ndi anayi. Anakuta mʼkati mwake ndi golide wosalala wolemera matani makumi awiri. Onani mutuwo |