Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 3:16 - Buku Lopatulika

16 Napanga maunyolo a m'chipinda chamkati, nawamanga pa mitu ya nsanamirazi, napanga makangaza zana limodzi, nawamanga pamaunyolo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Napanga maunyolo a m'chipinda chamkati, nawamanga pa mitu ya nsanamirazi, napanga makangaza zana limodzi, nawamanga pamaunyolo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Adapanga maunyolo okometsera, ofanafana ndi aja a m'kati mwa Nyumba ya Chauta, naŵaika pamwamba pa nsanamirazo. Adapanganso zinthu zonga makangaza zokwanira 100, ndipo adaziika ku maunyolowo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Iye anapanga maunyolo olumikizanalumikizana ndipo anawayika pamwamba pa zipilalazo. Anapanganso makangadza 100 ndipo anawalumikiza ku maunyolo aja.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 3:16
6 Mawu Ofanana  

Momwemo Solomoni anakuta m'kati mwa nyumba ndi golide woyengetsa, natambalika maunyolo agolide chakuno cha chipinda chamkati, namukuta ndi golide.


Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwake mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga ndanda mutu winawo.


Ndipo anapanga ku khomo la nyumba nsanamira ziwiri za mikono makumi atatu mphambu ziwiri; ndi mutu unakhala pamwamba pa iliyonse ndiwo mikono isanu.


Ndipo anaimiritsa nsanamirazo pakhomo pa Kachisi; imodzi ku dzanja lamanja, ndi inzake ku dzanja lamanzere; nalitcha dzina la iyi ya ku dzanja lamanja Yakini, ndi dzina la iyi ya ku dzanja lamanzere Bowazi.


nsanamira ziwiri, ndi zikhozo, ndi mitu iwiri inali pamwamba pa nsanamirazo, ndi maukonde awiri akukuta zikho ziwiri za mitu ili pamwamba pa nsanamirazo,


ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwa; mizere iwiri ya makangaza ya ukonde uliwonse, akukuta zikho ziwiri za mitu, inali pa nsanamirazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa